KULENGEZA ZOTSATIRA ZA KAWUNIWUNI WA MOMWE NTCHITO YOMANGA MA SIKIMU A LINGONI KOMANSO NKHULAMBE/WOWO ZINGAKHUDZIRE CHILENGEDWE KOMANSO UMOYO WA ANTHU
Boma la Malawi kudzera ku Unduna waza Ulimi lalandira ngongole komanso thandizo la ndalama kuchokera ku Bungwe la International Fund for Agriculture Development (IFAD) zomangira ma sikimu kudzera ku Pulojekiti ya PRIDE. Boma la Malawi lalandiranso thandizo la ndalama kuchokera ku Bungwe la Global Environmental Facility (GEF) zogwilira ntchito yolimbikitsa ntchito za ulimi yotchedwa ERASP. Unduna waza Ulimi kudzera ku Nthambi ya Ulimi Wanthilira ukufuna kugwiritsa ntchito mbali ina ya ndalamazi kukonza ma pulani komanso kumanga ma Sikimu a Lingoni m’boma la Machinga komanso Nkhulambe/Wowo m’boma la Phalombe.